LetsSingIt the internet lyrics database
en
0
picture

"Kuzizira" Lyrics

5.0 / 5
Song updated, review now!
Kukumazizira kukada
Tsiku kuchedwa kutha kukacha
Tsiku lonse mvula mawawa
Sindingachedwe ndidziwe za mawa
Mano anga anthu sawaona
Sikweni kweni kusekelera
Usiku zindivuta kugona
Ngati udzudzu ndimachezera
Moyo wathu dzana unkakoma
Kachikondi kutsekemera
Ubwino opanda mwina 'pena koma
Kachikondi kulemelera

CHORUS
Alipo akukukonda?
Alipo akukuhoda?
Alipo akukugwira?
Ndikungoganizira eya
Alipo akukuwuza amakukonda kuposa ine? ey
Poti dziko langa likuzizira popanda iwe yeah

VERSE TWO
Chikondi chinali on point
Ngati nyimbo yolondola ma note
Chinali perfect chinalibe fault
Anthu wokamba ankati tiri hot
Zoti chikondi chimawawa inali mphekesera
Anthu ena akamakamba tinkangomvetsera
Anthu akaduka kusowa chotigwetsera
Koma lero tandiona ndingo fwenthera
Maso anga ayandama in tears
Mtima wanga udzadza ndi fear
Usaganize zoti undisiye
Ndikungoganizira

CHORUS
Alipo akukukonda?
Alipo akukuhoda?
Alipo akukugwira?
Ndikungoganizira eya
Alipo akukuwuza amakukonda kuposa ine? ey
Poti dziko langa likuzizira popanda iwe yeah

VERSE THREE
Kodi chikondi nnakupatsa chija nchokwanira?
Kuti udzadikira mpaka nthawi idzakwanira?
Ngakhale moto utawotcha udzakakamira?
Chikondi chako chikuthawa kodi udzambwandira?
Ndiwe wekha ndikufuna mdziko langa dear
Mtima wako usakayike ndiwe wanga dziwa
Ndi pemphero langa nthawi zonse ukumbukira
Ndi kwa iwe kokha komwe mtima wanga ugundira

CHORUS
Alipo akukukonda?
Alipo akukuhoda?
Alipo akukugwira?
Ndikungoganizira eya
Alipo akukuwuza amakukonda kuposa ine? ey
Poti dziko langa likuzizira popanda iwe yeah
song info:
Verified yes
Language
Genre
Rank
Duration
Charts
Copyright ©
Writer
Lyrics licensed byLyricFind
AddedMarch 5th, 2013
Last updatedMarch 6th, 2022
About

Album Details

Video

Songs you may also like

Langwan Piksy
Similar genre
Popular on LetsSingIt
New on LetsSingIt
show all Langwan Piksy songs
show more songs with similar genre
show this week's top 1000 most popular songs
show all recently added songs

Contributors

leaderboard
activity

Comments (0)